Galatians 5:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu amene mukuyesa kusanduka olungama pakutsata Malamulowo, mudadzipatula nokha kusiya Khristu. Pamenepo mudalekana ndi madalitso aulere a Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mulibe kanthu ndi Khristu, inu amene muyesedwa olungama ndi lamulo; mudagwa posiyana nacho chisomo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu amene mukufuna kulungamitsidwa ndi lamulo mwachotsedwa mwa Khristu; munagwa kusiyana nacho chisomo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mulibe kanthu ndi Kristu, inu amene muyesedwa olungama ndi lamulo; mudagwa posiyana naco cisomo.