Galatians 6:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aliyense aziyesa yekha ntchito zake m'mene ziliri. Ngati zili bwino, adzatha kunyadira chifukwa cha ntchito zake zokhazo, osati chifukwa zapambana ntchito za mnzake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma yense ayesere ntchito yake ya iye yekha, ndipo pamenepo adzakhala nako kudzitamandira chifukwa cha iye yekha, si chifukwa cha wina.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthu aliyense aziyesa yekha ntchito zake mmene zilili. Ngati zili bwino, adzatha kunyadira chifukwa cha ntchito zake zokhazo, iyeyo asadzifanizire ndi munthu wina wake,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma yense ayesere nchito yace ya iye yekha, ndipo pamenepo adzakhala nako kudzitamandira cifukwa ca iye yekha, si cifukwa ca wina,