Genesis 1:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adati, “Panthaka pamere zomera zobala njere, ndiponso mitengo yobala zipatso zanjere malinga ndi mtundu wake,” ndipo zidachitikadi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mulungu ndipo anati, Dziko lapansi limere udzu, therere lobala mbeu, ndi mtengo wazipatso wakubala zipatso monga mwa mtundu wake, momwemo muli mbeu yake, pa dziko lapansi: ndipo kunatero.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Mulungu anati, “Dziko libereke zomera zobala mbewu, mitengo yobala zipatso za mbewu, molingana ndi mitundu yake.” Ndipo zinachitikadi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mulungu ndipo anati, Dziko lapansi limere maudzu, therere lobala mbeu, ndi mtengo wazipatso wakubala zipatso monga mwa mtundu wace, momwemo muli mbeu yace, pa dziko lapansi: ndipo kunatero.