Genesis 1:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero panthaka padamera zomera za mitundu yonse, zipatso zokhala ndi njere ndi mitengo yobeleka zipatso za njere, malingana ndi mitundu yao. Mulungu adaona kuti zinali zabwino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo dziko lapansi linamera udzu, therere lobala mbeu monga mwa mtundu wake, ndi mtengo wakubala zipatso, momwemo muli mbeu yake, monga mwa mtundu wake; ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Dziko linabereka zomera zokhala ndi mbewu monga mwa mitundu yake ndi mitengo yokhala ndi zipatso za mbewu mʼkati mwake monga mwa mitundu yake. Ndipo Mulungu anaona kuti zinali bwino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo dziko lapansi linamera maudzu, therere lobala mbeu monga mwa mtundu wace, ndi mtengo wakubala zipatso, momwemo muli mbeu yace, monga mwa mtundu wace; ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino.