Genesis 1:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero Mulungu adalenga nsomba zazikulu zam'nyanja, pamodzi ndi zolengedwa zina zonse zokhala m'madzi, ndiponso mbalame ndi zouluka zina zamitundumitundu. Mulungu adaona kuti zonse zimene adalengazo zinali zabwino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mulungu ndipo adalenga zinsomba zazikulu ndi zoyendayenda zamoyo zakuchuluka m'madzi mwa mitundu yao, ndi mbalame zamapiko, yonse monga mwa mtundu wake: ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Mulungu analenga zamoyo zikuluzikulu za mʼnyanja ndi chamoyo chamtundu uliwonse chokhala mʼmadzi ndi mbalame iliyonse ya mapiko monga mwa mtundu wake. Mulungu anaona kuti zinali bwino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mulungu ndipo adalenga zinsomba zazikuru ndi zoyendayenda zamoyo zakucuruka m'madzi mwa mitundu yao, ndi mbalame zamapiko, yonse monga mwa mtundu wace: ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino.