Genesis 1:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pomwepo Mulungu adalenga nyama zakuthengo potsata mitundu yake, ndi nyama zoŵeta potsata mitundu yake, ndiponso zokwaŵa zonse potsata mitundu yake. Mulungu adaona kuti zonse zimene adalengazo zinali zabwino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mulungu anapanga zinyama za dziko lapansi monga mwa mitundu yao; ndi ng'ombe monga mwa mtundu wake, ndi zonse zokwawa pansi monga mwa mitundu yao; ndipo Mulungu anaona kuti kunali kwabwino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mulungu anapanga nyama zakuthengo monga mwa mitundu yawo, nyama zoweta monga mwa mitundu yawo ndi nyama zokwawa monga mwa mitundu yawo. Ndipo Mulungu anaona kuti zinali bwino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mulungu anapanga zinyama za dziko lapansi monga mwa mitundu yao; ndi ng'ombe monga mwa mtundu wace, ndi zonse zakukwawa pansi monga mwa mitundu yao; ndipo Mulungu anaona kuti kunali kwabwino.