Genesis 1:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zitatha izo Mulungu adati, “Tiyeni tipange munthu m'chifanizo chathu, adzakhale wonga Ifeyo. Adzalamulire nsomba zam'nyanja, mbalame zamumlengalenga, nyama zoŵeta, ndi zokwaŵa zonse za pa dziko lapansi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati Mulungu, Tipange munthu m'chifanizo chathu, monga mwa chikhalidwe chathu: alamulire pa nsomba za m'nyanja, ndi pa mbalame za m'mlengalenga, ndi pa ng'ombe, ndi pa dziko lonse lapansi, ndi pa zokwawa zonse zakukwawa pa dziko lapansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zitatha izi Mulungu anati, “Tipange munthu mʼchifanizo chathu, mofanana ndi ife kuti alamulire nsomba za mʼnyanja, mbalame zamlengalenga, nyama zonse zoweta ndi zonse zokwawa za pa dziko lapansi ndi zamoyo zonse zakutchire.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati Mulungu, Tipange munthu m'cifanizo cathu, monga mwa cikhalidwe cathu: alamulire pa nsomba za m'nyanja, ndi pa mbalame za m'mlengalenga, ndi pa ng'ombe, ndi pa dziko lonse lapansi, ndi pa zokwawa zonse zakukwawa pa dziko lapansi.