Genesis 1:28 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adaŵadalitsa poŵauza kuti, “Mubereke ndi kuchulukana, mudzaze dziko lonse lapansi ndi kumalilamulira. Ndakupatsani ulamuliro pa nsomba, mbalame ndi nyama zonse zimene zikukhala pa dziko lapansi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pa nsomba za m'nyanja, ndi pa mbalame za m'mlengalenga, ndi zamoyo zonse zakukwawa pa dziko lapansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mulungu anawadalitsa nati kwa iwo, “Muberekane, muchulukane, mudzaze dziko lapansi ndipo muligonjetse. Mulamulire nsomba zamʼnyanja, mbalame zamlengalenga ndi cholengedwa chamoyo chilichonse chimene chimayenda mokwawa pa dziko lapansi.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, mucuruke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pa nsomba za m'nyanja, ndi pa mbalame za m'mlengalenga, ndi pa zamoyo zonse zakukwawa pa dziko lapansi.