Genesis 1:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo Mulungu adati, “Ndikukupatsani zomera zonse za mtundu wokhala njere, ndi mitundu yonse ya zomera zobala zipatso zanjere, kuti muzidya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati Mulungu, Taonani, ndakupatsani inu therere lonse lakubala mbeu lili pa dziko lapansi, ndi mitengo yonse m'mene muli chipatso cha mtengo wakubala mbeu; chidzakhala chakudya cha inu:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Mulungu anati, “Ine ndakupatsani chomera chilichonse cha pa dziko lapansi chimene chili ndi mbewu komanso mtengo uliwonse wobala zipatso zokhala ndi mbewu mʼkati mwake kuti zikhale chakudya chanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati Mulungu, Taonani, ndakupatsani inu therere lonse lakubala mbeu liri pa dziko lapansi, ndi mitengo yonse m'mene muli cipatso ca mtengo wakubala mbeu; cidzakhala cakudya ca inu: