Genesis 10:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Eberi anali ndi ana aŵiri. Wina anali Pelegi, chifukwa pa nthaŵi ya moyo wake, anthu onse a pa dziko lapansi anali ogaŵikana. Dzina la mbale wake linali Yokotani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kwa Eberi ndipo kunabadwa ana amuna awiri; dzina la wina ndi Pelegi; chifukwa kuti m'masiku ake dziko lapansi linagawanikana; dzina la mphwake ndi Yokotani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
A Eberi anabereka ana aamuna awiri: Wina anamutcha Pelegi chifukwa pa nthawiyo anthu a pa dziko lapansi anagawikana. Dzina la mʼbale wake linali Yokitani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kwa Ebere ndipo kunabadwa ana amuna awiri; dzina la wina ndi Pelege; cifukwa kuti m'masiku ace dziko lapansi linagawanikana; dzina la mphwace ndi Yokitani.