Genesis 11:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Abramu ndi Nahori adakwatira. Abramu adakwatira Sarai, ndipo Nahori adakwatira Milika mwana wa Harani, amene analinso bambo wake wa Isika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Abramu ndi Nahori, anadzitengera okha akazi; dzina lake la mkazi wa Abramu ndilo Sarai; ndi dzina lake la mkazi wa Nahori ndilo Milika, mwana wake wa Harani, atate wake wa Milika, ndi atate wake wa Isika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abramu ndi Nahori onse anakwatira. Dzina la mkazi wa Abramu linali Sarai, ndipo la mkazi wa Nahori linali Milika. Iyeyu ndi Isika abambo awo anali Harani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Abramu ndi Nahori, anadzitengera okha akazi; dzina lace la mkazi wa Abramu ndilo Sarai; ndi dzina lace la mkazi wa Nahori ndilo Milika, mwana wace wa Harana, atate wace wa Milika, ndi atate wace wa Yisika.