Genesis 11:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adayamba kuuzana kuti, “Tiyeni tiwumbe njerwa ndi kuzitentha.” Motero m'malo mwa miyala adatenga njerwa, namangira phula m'malo mwa matope.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ananenana wina ndi wina, Tiyeni tipange njerwa, tiziochetse. Ndipo anali ndi njerwa naziyesa miyala, ndi katondo anayesa matope.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono anawuzana kuti, “Tiyeni tiwumbe njerwa ndi kuziwotcha bwinobwino.” Tsono mʼmalo mwa miyala anagwiritsa ntchito njerwa zowotcha, ndipo mʼmalo mwa matope anagwiritsa ntchito phula.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ananenana wina ndi wina, Tiyeni tipange njerwa, tiziocetse. Ndipo anali ndi njerwa naziyesa miyala, ndi katondo anayesa matope.