Genesis 11:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Tera adatenga mwana wake Abramu ndi Loti mdzukulu wake, mwana wa Harani, ndiponso mpongozi wake Sarai, mkazi wa Abramu. Adanyamuka ulendo kuchoka ku mzinda uja wa Uri wa ku Kaldeya napita nawo ku dziko la Kanani. Adakafika ku Harani, nakhazikika kumeneko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Tera anatenga Abramu mwana wake wamwamuna, ndi Loti mwana wa Harani, mwana wake wamwamuna, ndi Sarai mpongozi wake, mkazi wa mwana wake Abramu; ndipo anatuluka pamodzi nao ku Uri wa kwa Akaldeya kuti amuke ku dziko la Kanani, ndipo anafika ku Harani, nakhala kumeneko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tera anatenga mwana wake Abramu, mdzukulu wake Loti, ndi mpongozi wake Sarai, mkazi wa Abramu natuluka mzinda wa Uri wa ku Akaldeya kupita ku Kanaani. Pamene anafika ku Harani, anakhazikika kumeneko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Tera anatenga Abramu mwana wace wamwamuna, ndi Loti mwana wa Harana, mwana wace wamwamuna, ndi Sarai mpongozi wace, mkazi wa mwana wace Abramu; ndipo anaturuka pamodzi nao ku Uri wa kwa Akaldayo kuti amuke ku dziko la Kanani, ndipo anafika ku Harana, nakhala kumeneko.