Genesis 11:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo adati, “Tsopano anthu onseŵa ndi amodzi, ndipo akulankhula chilankhulo chimodzi. Zinthu akuchitazi ndi chiyambi chabe cha zimene adzachite. Kenaka iwoŵa adzachita chilichonse chimene afuna.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anati, Taonani, anthu ali amodzi, ndipo onse ali nacho chinenedwe chao chimodzi; ndipo ichi ayamba kuchita: ndipo tsopano palibe kanthu kakuletsedwa nao kamene akafuna kuchita.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anati, “Anthuwa ndi amodzi, ndipo ali ndi chiyankhulo chimodzi. Izi akuchitazi nʼchiyambi chabe cha zomwe akufuna kukwaniritsa kuchita.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anati, Taonani, anthu ali amodzi, ndipo onse ali naco cinenedwe cao cimodzi; ndipo ici ayamba kucita: ndipo tsopano palibe kanthu kakuletsedwa nao kamene akafuna kucita.