Genesis 11:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho mzinda umenewo adautcha Babele, chifukwa choti kumeneko Chauta adasokoneza chilankhulo cha anthu onse. Ndipo kuchokera kumeneko adaŵamwaza anthuwo pa dziko lonse lapansi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake anatcha dzina lake Babele; pakuti kumeneko Yehova anasokoneza chinenedwe cha dziko lonse lapansi; kuyambira pamenepo Yehova anabalalitsa iwo pa dziko lonse lapansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake mzindawo unatchedwa Babeli, popeza Yehova anasokoneza chiyankhulo cha anthu onse. Powachotsa kumeneko, Yehova anawabalalitsira pa dziko lonse lapansi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace anacha dzina lace Babele; pakuti kumeneko Yehova anasokoneza cinenedwe ca dziko lonse lapansi; kuyambira pamenepo Yehova anabalalitsa iwo pa dziko lonse lapansi.