Genesis 12:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma m'dziko limenelo mudagwa njala. Ndipo chifukwa choti njala idaakula kwambiri, Abramu adapitirira ndithu chakumwera, mpaka kukafika ku Ejipito, nakhala kumeneko kanthaŵi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo munali njala m'dzikomo, ndipo anatsikira Abramu ku Ejipito kukakhala kumeneko, chifukwa kuti njala inali yaikulu m'dziko m'menemo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kunagwa njala yayikulu mʼdzikomo, ndipo Abramu anapita ku Igupto kukakhala ngati mlendo kwa kanthawi kochepa popeza njalayo inakula kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo munali njala m'dzikomo, ndipo anatsikira Abramo ku Aigupto kukakhala kumeneko, cifukwa kuti njala inali yaikuru m'dziko m'menemo.