Genesis 12:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akalonga a mfumu ya ku Ejipito atamuwona mkaziyo, adakauza Farao za kukongola kwake. Pomwepo anthu aja adamtenga mkaziyo kukamuika ku nyumba ya mfumu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo akalonga ake a Farao anamuona iye, namyamikira iye kwa Farao; ndipo anamuka ndi mkazi kunyumba kwake kwa Farao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene akuluakulu a ku nyumba ya Farao anamuona, anakamuyamikira pamaso pa Farao ndipo ananka naye ku nyumba ya Farao.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo akaronga ace a Farao anamuona iye, namyamikira iye kwa Farao; ndipo anamuka ndi mkazi kunyumba kwace kwa Farao.