Genesis 12:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo Farao adamchitira zabwino Abramu uja chifukwa cha mkaziyo, nampatsa nkhosa, mbuzi, ng'ombe, abulu, ngamira ndiponso akapolo aamuna ndi aakazi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anamchitira Abramu bwino chifukwa cha iyeyo; ndipo anali nazo nkhosa, ndi ng'ombe, ndi abulu, ndi akapolo, ndi adzakazi, ndi abulu akazi, ndi ngamira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abramu naye zinthu zinkamuyendera bwino chifukwa cha Sarai. Farao anamupatsa nkhosa, ngʼombe, abulu aamuna ndi abulu aakazi, antchito aakazi pamodzi ndi ngamira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anamcitira Abramu bwino cifukwa ca iyeyo; ndipo anali nazo nkhosa, ndi ng'ombe, ndi aburu, ndi akapolo, ndi adzakazi, ndi aburu akazi, ndi ngamila.