Genesis 12:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Abramu adatenga mkazi wake Sarai, Loti mwana wa mng'ono wake, pamodzi ndi chuma chake chonse, ndi antchito amene adaali nawo ku Harani. Adayamba ulendo wonka ku Kanani. Atafika ku Kanani,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Abramu anatenga Sarai mkazi wake, ndi Loti mwana wa mphwake, ndi chuma chao chimene anasonkhanitsa, ndi miyoyo imene anabala m'Harani; natuluka kunka ku dziko la Kanani, ndipo anadza ku dziko la Kanani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abramu anatenga mkazi wake Sarai, Loti, mwana wamngʼono wake, pamodzi ndi chuma chawo chimene anapeza ndi antchito amene anali nawo ku Harani. Iwo ananyamuka ulendo mpaka kukafika ku dziko la Kanaani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Abramu anatenga Sarai mkazi wace, ndi Loti mwana wa mphwace, ndi cuma cao cimene anasonkhanitsa, ndi miyoyo imene anabala m'Harana; naturuka kunka ku dziko la Kanani, ndipo anadza ku dziko la Kanani.