Genesis 12:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake adasendera ku mapiri a kuvuma kwa Betele, ndipo adamanga hema lake pakati pa Betele chakuzambwe ndi Ai chakuvuma. Kumenekonso adamangako guwa, ndipo adatama dzina la Chauta mopemba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iye anachoka kumeneko kunka kuphiri la kum'mawa kwa Betele, namanga hema wake; Betele anali kumadzulo, ndi Ai anali kum'mawa: kumeneko ndipo anammangira Yehova guwa la nsembe, naitanira dzina la Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atachoka pamenepo analowera cha ku mapiri a kummawa kwa Beteli namangako tenti yake pakati pa Beteli chakumadzulo ndi Ai chakummawa. Kumeneko anamangira Yehova guwa lansembe napemphera mʼdzina la Yehovayo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye anacoka kumeneko kunka ku phiri la kum'mawa kwa Beteli, namanga hema wace; Beteli anali kumadzulo, ndi Ai anali kum'mawa: kumeneko ndipo anammangira Yehova guwa la nsembe, naitanira dzina la Yehova.