Genesis 13:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero Loti atayang'anayang'ana, adaona kuti chigwa chonse cha mtsinje wa Yordani mpaka ku Zowari chili ndi madzi ambiri. Chigwacho chinali ngati munda wa Chauta kapenanso ngati dziko la Ejipito. Nthaŵi imeneyi nkuti Chauta asanaononge mizinda ya Sodomu ndi Gomora.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Loti anatukula maso ake nayang'ana chigwa chonse cha Yordani kuti chonsecho chinali ndi madzi ambiri, asanaononge Yehova Sodomu ndi Gomora, monga munda wa Yehova, monga dziko la Ejipito pakunka ku Zowari.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Loti atamwazamwaza maso anaona kuti chigwa chonse cha mtsinje wa Yorodani chinali chothiriridwa bwino ngati munda wa Yehova, kapena ngati dziko la ku Igupto mpaka ku Zowari. (Nthawi iyi nʼkuti Yehova asanawononge Sodomu ndi Gomora).
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Loti anatukula maso ace nayang'ana cigwa conse ca Yordano kuti conseco cinali ndi madzi ambiri, asanaononge Yehova Sodomu ndi Gomora, monga munda wa Yehova, monga dziko la Aigupto pakunka ku Zoari.