Genesis 13:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Loti adadzisankhira chigwa chonse cha Yordani, napita kukakhala chakuvuma. Umu ndimo m'mene anthu aŵiriwo adasiyanirana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Loti anasankha chigwa chonse cha Yordani; ndipo Loti anachoka ulendo wake kunka kum'mawa: ndipo analekana wina ndi mnzake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Loti anadzisankhira yekha chigwa chonse cha Yorodani nanyamuka kulowera cha kummawa. Choncho anthu awiriwa anasiyana.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Loti anasankha cigwa conse ca Yordano; ndipo Loti anacoka ulendo wace kunka kum'mawa: ndipo analekana wina ndi mnzace.