Genesis 13:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Abramu adakhala m'dziko la Kanani, koma Loti adakhazikika pakati pa mizinda yam'chigwa, nakamanga hema pafupi ndi mzinda wa Sodomu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Abramu anakhala m'dziko la Kanani, ndipo Loti anakhala m'midzi ya m'chigwa, nasendeza hema wake kufikira ku Sodomu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abramu anakhala mʼdziko la Kanaani, pamene Loti anakakhala pakati pa mizinda ikuluikulu ya mʼchigwamo. Anamanga tenti yake pafupi ndi Sodomu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Abramu anakhala m'dziko la Kanani, ndipo Loti anakhala m'midzi ya m'cigwa, nasendeza hema wace kufikira ku Sodomu.