Genesis 13:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero Abramu adazula hema lake, nakakhala patsinde pa mitengo ya thundu ya ku Mamure, imene ili ku Hebroni. Ndipo kumeneko adamangira Chauta guwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Abramu anasuntha hema wake nafika nakhala pa mitengo yathundu ya pa Mamure, imene ili m'Hebroni, nammangira Yehova kumeneko guwa la nsembe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Abramu anasamutsa tenti yake napita kukakhala pafupi ndi mitengo ikuluikulu ija ya thundu ya ku Mamre ku Hebroni, kumene anamangira Yehova guwa lansembe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Abramu anasuntha hema wace nafika nakhala pa mitengo yathundu ya pa Mamre, imene iri m'Hebroni, nammangira Yehova kumeneko guwa la nsembe.