Genesis 13:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kuchokera kumwera adasendera ndithu cha ku Betele, ku malo aja kumene kale adaamangako hema lake, pakati pa Betele ndi Ai.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anankabe ulendo wake kuchokera ku dziko la kumwera kunka ku Betele, kufikira kumalo kumene kunali hema wake poyamba paja pakati pa Betele ndi Ai;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atachoka ku Negevi, anayenda malo osiyanasiyana mpaka anafika ku Beteli, ku malo a pakati pa Beteli ndi Ai, kuja kumene anamanga tenti poyamba,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anankabe ulendowace kucokera ku dziko la kumwera kunka ku Beteli, kufikira kumalo kumene kunali hema wace poyamba paja, pakati pa Beteli ndi Ai;