Genesis 14:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chigwa cha Sidimu chinali chodzaza ndi maenje a phula. Tsono anthu a ku Sodomu ndi Gomora adagonja nathaŵa nkhondo, ndipo adagwa m'maenjemo, koma ena adathaŵira ku mapiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chigwa cha Sidimu chinali ndi zitengetenge thoo; ndipo anathawa mafumu a ku Sodomu ndi Gomora nagwa m'menemo: amene anatsala anathawira kuphiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Chigwa cha Sidimu chinali chodzaza ndi maenje aphula. Choncho pamene mafumu a ku Sodomu ndi Gomora amathawa, ankhondo ena anagweramo ndipo ena anathawira ku mapiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cigwa ca Sidimu cinali ndi zitengetenge tho; ndipo anathawa mafumu a ku Sodomu ndi Gomora nagwa m'menemo: amene anatsala anathawira kuphiri.