Genesis 14:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma munthu wina atapulumuka, adabwera kwa Abramu Muhebri uja, namuuza zonsezi. Abramuyo ankakhala pafupi ndi mitengo ija ya thundu ya ku Mamure, wa fuko la Amoni, mbale wa Esikolo ndi Anere, amene ankagwirizana ndi Abramu pa nkhondo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anadza wina amene anapulumuka namuuza Abramu Muhebri; ndipo iye analinkukhala pa mitengo yathundu ya pa Mamure Mwamori, mkulu wake wa Esikolo, ndi mkulu wake wa Anere; amenewo ndiwo opangana naye Abramu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma munthu wina amene anathawa, anabwera kudzamufotokozera Abramu Mhebri. Tsono Abramu ankakhala pafupi ndi mitengo ikuluikulu ya thundu ya Mamre wa fuko la Aamori, mʼbale wake wa Esikolo ndi Aneri. Onsewa anali pa mgwirizano ndi Abramu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anadza wina amene anapulumuka namuuza Abramu Mhebri; ndipo iye analinkukhala pa mitengo yathundu ya pa Mamre M-amori, mkuru wace wa Esakolo, ndi mkuru wace wa Aneri; amenewo ndiwo opangana naye Abramu.