Genesis 14:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
ndipo adaŵalanda zao zonse. Adabwera naye Loti, mwana wa mbale wake, pamodzi ndi zake zonse, kuphatikizapo akazi ndi anthu ena onse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anabwera nacho chuma chonse, nabwera naye Loti yemwe ndi chuma chake, ndi akazi ndi anthu omwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo anawalanda katundu wawo yense nabwera naye Loti, katundu wake yense, pamodzi ndi akazi ndi anthu ena.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anabwera naco cuma conse, nabwera naye Loti yemwe ndi cuma cace, ndi akazi ndi anthu omwe.