Genesis 14:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene Abramu ankabwera kuchokera kumene adakagonjetsa Kedorilaomere ndi mafumu ena ogwirizana naye aja, mfumu ya ku Sodomu idatuluka kukakumana naye ku Chigwa cha Save (ndiye kuti Chigwa cha Mfumu).
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anatuluka mfumu ya Sodomu kukomana naye, atabwera anatha kuwakantha Kedorilaomere ndi mafumu amene anali naye, ku chigwa cha Save (ndiko ku chigwa cha mfumu),
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abramu atabwerera kuchokera kogonjetsa Kedorilaomere ndi mafumu amene anali nawo pa mgwirizano, mfumu ya ku Sodomu inabwera kudzakumana naye ku Chigwa cha Save (chimenechi ndicho Chigwa cha Mfumu).
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anaturuka mfumu ya Sodomu kukomana naye, atabwera anatha kuwakantha Kedorelaomere ndi mafumu amene anali naye, ku cigwa ca Save (ndiko ku cigwa ca mfumu),