Genesis 14:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atamandike Mulungu Wopambanazonse, amene adakupatsa mphamvu zogonjetsera adani ako onse.” Pamenepo Abramu adapereka kwa Melkizedeki chigawo chachikhumi cha zinthu zonse zimene adaalanda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ayamikike Mulungu Wamkulukulu amene wapereka adani ako m'dzanja lako. Ndipo anampatsa iye limodzi la magawo khumi la zonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo adalitsike Mulungu Wammwambamwamba amene anapereka adani ako mʼdzanja lako.” Ndipo Abramu anamupatsa iye chakhumi cha zonse anali nazo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ayamikike Mulungu Wamkurukuru amene wapereka adani ako m'dzanja lako. Ndipo anampatsa iye limodzi la magawo khumi la zonse.