Genesis 14:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Sinditenga kalikonse ai. Nditengako zokhazo zimene anyamata anga adadya, ndi zoyenera kugaŵira amene adandiperekeza, monga Anere, Esikolo ndi Mamure. Iwo atengeko magawo ao.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma chokhachi anadya anyamata, ndi gawo lao la anthu amene ananka pamodzi ndi ine, Anere, Esikolo, ndi Mamure, iwo atenge gawo lao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sindidzalandira kanthu kalikonse kupatula zokhazo zimene anthu anga adya ndi gawo la katundu la anthu amene ndinapita nawo monga Aneri, Esikolo ndi Mamre. Iwowa atenge gawo lawo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma cokhaci anadya anyamata, ndi gawo lao la anthu amene ananka pamodzi ndi ine, Aneri, Esikolo, ndi Mamre, iwo atenge gawo lao.