Genesis 14:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo adapotoloka, nakafika ku Enimisipati (ndiye kuti Kadesi), ndipo adagonjetsa dziko lonse la Aamaleke pamodzi ndi la Aamori amene ankakhala ku Hazazoni-Tamara.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anabwera nafika ku Enimisipati (kumeneko ndi ku Kadesi), nakantha dziko lonse la Aamaleke, ndiponso Aamori amene akhala m'Hazazoni-Tamara.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka anabwerera napita ku Eni-Misipati (ku Kadesi), ndipo anagonjetsa dera lonse la Aamaleki, kuphatikizanso Aamori amene ankakhala ku Hazazoni Tamara.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anabwera nafika ku Eni-Misipati (ku meneko ndi ku Kadese), nakantha dziko lonse la Aamaleki, ndiponse Aamori amene akhala m'Hazezoni-tamara.