Genesis 15:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zitatha izi, Chauta adaonekera Abramu m'masomphenya namuuza kuti, “Usachite mantha Abramu, Ine ndili ngati chishango chako chokutchinjiriza. Mphotho yako idzakhala yaikulu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Zitapita izo, mau a Yehova anadza kwa Abramu m'masomphenya, kuti, Usaope, Abramu, Ine ndine chikopa chako ndi mphotho yako yaikulukulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zitatha izi, Yehova anayankhula ndi Abramu mʼmasomphenya nati: “Usaope Abramu. Ine ndili ngati chishango chokutchinjiriza. Mphotho yako idzakhala yayikulu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Zitapita izo, mau a Yehova anadza kwa Abramu m'masomphenya, kuti, Usaope, Abramu, Ine ndine cikopa cako ndi mphotho yako yaikurukuru.