Genesis 15:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene dzuŵa linkaloŵa, Abramu adagwidwa ndi tulo tofanato, ndiponso adachita mantha kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo linalinkulowa dzuwa, ndi tulo tatikulu tinamgwera Abramu: ndipo taonani, kuopsa kwa mdima waukulu kunamgwera iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene dzuwa limalowa Abramu anagona tulo tofa nato ndipo mdima wandiweyani ndi wochititsa mantha unamuphimba.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo linalinkulowa dzuwa, ndi tulo tatikuru tinamgwera Abramu: ndipo taonani, kuopsya kwa mdima waukuru kunamgwera iye.