Genesis 15:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa tsiku limeneli mpamene Chauta adachita chipangano ndi Abramu nati, “Ndikulonjeza kuti ndidzapatsa zidzukulu zako dziko lonseli kuyambira ku mtsinje wa ku Ejipito mpaka ku mtsinje waukulu wa Yufurate.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsiku lomwelo Yehova anapangana chipangano ndi Abramu, nati, Ndidzapatsa mbeu zako dziko ili, kuyambira pa mtsinje wa ku Ejipito kufikira pa mtsinje waukulu, mtsinje wa Yufurate:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa tsiku limenelo, Yehova anachita pangano ndi Abramu nati, “Ndikulonjeza kuti ndidzapereka dziko ili kwa zidzukulu zako, kuchokera ku mtsinje wa ku Igupto mpaka ku mtsinje waukulu wa Yufurate.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsiku lomwelo Yehova anapangana cipangano ndi Abramu, nati, Ndidzapatsa mbeu zako dziko ili, kuyambira pa nyanja ya Aigupto kufikira pa nyanja yaikuru, nyanja ya Firate: