Genesis 15:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Chauta adamuuza kuti, “Uyu sadzalandira chuma chako kukhala choloŵa chake. Yemwe adzalandire chuma chakochi ndi mwana wako weniweni.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo, taonani, mau a Yehova anadza kwa iye kuti, Uyu sadzakhala wakulowa m'malo mwako; koma iye amene adzatuluka m'chuuno mwako, ndiye adzakhala wakulowa m'malo mwako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anayankhula naye nati: “Munthu uyu sadzalowa mʼmalo mwako, koma mwana wako weniweni wamwamuna, wobereka wekha ndiye adzalowe mʼmalo mwako.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo, taonani, mau a Yehova anadza kwa iye kuti, Uyu sadzakhala wakulowa m'malo mwako; koma iye amene adzaturuka m'cuuno mwako, ndiye adzakhala wakulowa m'malo mwako.