Genesis 15:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pomwepo Chauta adatulutsira Abramu panja, namuuza kuti, “Tayang'ana kuthamboku, ndipo uŵerenge nyenyezizo ngati ungathe. Iwe udzakhala ndi zidzukulu zochuluka ngati nyenyezizo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anamtulutsa iye kunja, nati, Tayang'anatu kumwamba, uwerenge nyenyezi, ngati ukhoza kuziwerenga zimenezo: ndipo anati kwa iye, Zoterezo zidzakhala mbeu zako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anapita naye Abramu panja nati, “Tayangʼana kumwambaku, ndipo chifukwa cha chimenechi uwerenge nyenyezi ngati ungathe kuziwerenga.” Ndipo anamuwuza kuti, “Ndi mmene adzakhalire ana ako ndi zidzukulu zako.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anamturutsa iye kunja, nati, Tayang'anatu kumwamba, uwerenge nyenyezi, ngati ukhoza kuziwerenga zimenezo: ndipo anati kwa iye, Zoterezo zidzakhala mbeuzako.