Genesis 16:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Popitiriza mau mngeloyo adati, “Tsopano uli pafupi kukhala ndi mwana wamwamuna, udzamutche Ismaele, ndiye kuti Chauta wamva kulira kwako pa zovuta zako.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa iye, Taona, uli ndi pakati, ndipo udzabala mwana wamwamuna; nudzamutcha dzina lake Ismaele; chifukwa Yehova anamva kusauka kwako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mngelo wa Yehova uja anamuwuzanso kuti, “Ndiwe woyembekezera ndipo udzabala mwana wamwamuna. Udzamutcha dzina lake Ismaeli, pakuti Yehova wamva kulira chifukwa cha kuzunzika kwako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa iye, Taona, uli ndi pakati, ndipo udzabala mwana wamwamuna; nudzamucha dzina lace Ismayeli; cifukwa Yehova anamva kusauka kwako.