Genesis 16:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma mwana wako adzakhala ndi mtima wa chilombo, adzadana ndi aliyense, ndipo anthu onse adzadana naye. Adzakhala akudana ndi abale ake onse.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iye adzakhala munthu wa m'thengo; ndipo dzanja lake lidzakhala lotsutsana ndi anthu onse, ndi manja a anthu onse adzakhala otsutsana naye: ndipo iye adzakhala pamaso pa abale ake onse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye adzakhala munthu wa khalidwe ngati mʼmbulu wamisala; adzadana ndi aliyense ndipo anthu onse adzadana naye, adzakhala mwaudani pakati pa abale ake onse.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye adzakhala munthu wa m'thengo; ndipo dzanja lace lidzakhala lotsutsana ndi anthu onse, ndi manja a anthu onse adzakhala otsutsana naye: ndipo iye adzakhala pamaso pa abale ace onse.