Genesis 16:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Hagara adatcha Chauta amene adalankhula naye kuti, “Inu ndinu Mulungu wondipenya,” poti adati, “Pano ndamuwona Iye amene amandipenya.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anatcha dzina la Yehova amene ananena naye, Ndinu Mulungu wakundiona ine; pakuti anati, Kodi kunonso ndayang'ana pambuyo pake pa Iye amene wakundiona ine?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Hagara anatcha Yehova amene anamuyankhula uja dzina loti: “Ndinu Mulungu amene mumandiona,” popeza anati, “Ndakumana ndi Yehova atatha kundikomera mtima.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anacha dzina la Yehova amene ananena naye, Ndinu Mulungu wakundiona ine; pakuti anati, Kodi kunonso ndayang'ana pambuyo pace pa iye amene wakundiona ine?