Genesis 16:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake anthu amachitchula chitsime cha pakati pa Kadesi ndi Beredi kuti Chitsime cha Wamoyo-Wondipenya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake chitsimecho chinatchedwa Beere-Lahai-Roi; taonani chili pakati pa Kadesi ndi Beredi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake chitsime chija chimene chili pakati pa Kadesi ndi Beredi chinatchedwa Beeri-lahai-roi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace citsimeco cinachedwa Beerelahai-roi; taonani ciri pakati pa Kadese ndi Berede.