Genesis 16:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Sarai adauza Abramu kuti, “Chauta sadandipatse ana. Bwanji osati muloŵane ndi mdzakazi wangayu kuti kapena nkundibalira mwana?” Abramu adavomereza zimenezo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Sarai anati kwa Abramu, Taonanitu, Yehova anandiletsa ine kuti ndisabale: lowanitu kwa mdzakazi wanga; kapena ndikalandire ndi iye ana. Ndipo Abramu anamvera mau a Sarai.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo Sarai anati kwa Abramu, “Yehova sanalole kuti ine ndikhale ndi ana. Bwanji mulowe mwa wantchito wanga wamkaziyu kuti mwina ndingaone ana kudzera mwa iyeyu.” Abramu anamvera Sarai.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Sarai anati kwa Abramu, Taonanitu, Yehova anandiletsa ine kuti ndisabale: lowanitu kwa mdzakazi wanga; kapena ndikalandire ndi iye ana. Ndipo Abramu anamvera mau a Sarai.