Genesis 16:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero Sarai adapereka Hagara uja kwa Abramu, kuti akhale mkazi wake wamng'ono. (Zimenezi zidachitika Abramu atakhala ku Kanani zaka khumi).
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Sarai mkazi wake wa Abramu anatenga Hagara mdzakazi wake wa ku Ejipito, Abramu atakhala m'dziko la Kanani zaka khumi, nampereka iye kwa Abramu mwamuna wake, kuti akhale mkazi wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Sarai anatenga Hagara wantchito wake wamkazi wa ku Igupto uja namupereka kwa Abramu mwamuna wake kuti akhale mkazi wake. Izi zinachitika Abramu atakhala ku Kanaani zaka khumi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Sarai mkazi wace wa Abramu anatenga Hagara mdzakazi wace wa ku Aigupto, Abramu atakhala m'dziko la Kanani zaka khumi, nampereka iye kwa Abramu mwamuna wace, kuti akhale mkazi wace.