Genesis 16:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku lina Sarai adauza Abramu kuti, “Cholakwa chimenechi chakuti Hagara akundinyoza, chili pa inu. Ine ndidakupatsani mdzakazi ameneyu, ndipo kuyambira paja adatenga pathupipa, wakhala akundinyoza. Chauta ndiye aweruze kuti tiwone wolakwa ndani pakati pathu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Sarai anati kwa Abramu, kusauka kwanga kukhale pa iwe: ndakupatsa iwe mdzakazi wanga pamtima pako; ndipo pakuona kuti anatenga pakati anandipeputsa ine m'maso mwake: Yehova aweruze pakati pa iwe ndi ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo Sarai anati kwa Abramu, “Inu ndinu amene mwandiputira nkhanza zikundichitikirazi. Ndinakupatsani wantchito wanga wamkazi kuti akhale mkazi wanu, ndiye tsopano wayamba kundinyoza ine chifukwa wadziwa kuti ndi woyembekezera. Yehova ndiye amene aweruze pakati pa inu ndi ine.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Sarai anati kwa Abramu, Kusauka kwanga kukhale pa iwe: ndakupatsa iwe mdzakazi wanga pamtima pako; ndipo pakuona kuti anatenga pakati anandipeputsa ine m'maso mwace: Yehova aweruze pakati pa iwe ndi ine.