Genesis 16:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Abramu adayankha kuti, “Iyeyu ndi mdzakazi wako, ndipo ali mu ulamuliro wako. Chita naye chilichonse chomwe ufuna.” Choncho Sarai adayamba kuzunza Hagara, mpaka Hagarayo adathaŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Abramu anati kwa Sarai, Taona, mdzakazi wako ali m'dzanja lako, umchitire iye chimene chikukomera m'maso mwako. Ndipo Sarai anamsautsa iye, ndipo anathawa kumaso kwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abramu anati, “Wantchito wakoyu ali mʼmanja mwako. Chita naye chilichonse chimene ukuganiza kuti ndi chokukomera.” Tsono Sarai anazunza Hagara mpaka anathawa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Abramu anati kwa Sarai, Taona, mdzakazi wako ali m'dzanja lako, umcitire iye cimene cikukomera m'maso mwako. Ndipo Sarai anamsautsa iye, ndipo anathawa kumaso kwace.