Genesis 17:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Muziwumbala mwana wamwamuna aliyense akakwanitsa masiku asanu ndi atatu. Muziwumbala mwamuna aliyense pa mibadwo yanu yonse, mbadwa kapena kapolo amene mudamgula kwa mlendo wosakhala wa mbumba yanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
A masiku asanu ndi atatu azidulidwa mwa inu, ana amuna onse m'mibadwo mwanu, amene abadwa m'nyumba ndi amene agulidwa ndi ndalama kwa alendo ali onse, wosakhala mwa mbeu zako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuyambira tsopano mpaka mibado ya mʼtsogolomo mwana wamwamuna aliyense pakati panu amene wakwana masiku asanu ndi atatu ayenera kuchita mdulidwe. Awa ndi ana obadwa mʼbanja lako, kapena akapolo ochita kugula ndi ndalama, mlendo osakhala wa mʼmbumba yako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
A masiku asanu ndi atatu azidulidwa mwa inu, ana amuna onse m'mibadwo mwanu, amene abadwa m'nyumba ndi amene agulidwa ndi ndalama kwa alendo ali onse, wosakhala mwa mbeu zako.