Genesis 17:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inde aliyense aumbalidwe, ndipo chimenechi chidzakhala chizindikiro pa matupi anu, choonetsa kuti chipangano changa ndi inu nchamuyaya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Azidulidwatu amene abadwa m'nyumba mwako ndi amene agulidwa ndi ndalama zako: ndipo pangano langa lidzakhala m'thupi mwako pangano losatha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Achite mdulidwe ndithu mwana wamwamuna aliyense, mbadwa ngakhale kapolo wochita kugula ndi ndalama, ndipo ichi chidzakhala chizindikiro pa thupi lanu cha pangano langa lamuyaya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Azidulidwatu amene abadwa m'nyumba mwako ndi amene agulidwa ndi ndalama zako: ndipo pangano langa lidzakhala m'thupi mwako pangano losatha.