Genesis 17:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iyeyu ndidzamdalitsa ndipo adzakubalira mwana wamwamuna. Ndidzamdalitsa, ndipo adzakhala mai wa mitundu ya anthu. Pakati pa zidzukulu zakezo padzatuluka mafumu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzamdalitsa iye, ndiponso ndidzakupatsa iwe mwana wamwamuna wobadwa mwa iye, inde, ndidzamdalitsa iye, ndipo adzakhala amake amitundu, mafumu a anthu adzatuluka mwa iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzamudalitsa ndipo adzakubalira mwana wamwamuna. Ndidzamudalitsa kuti akhale mayi wa mitundu ya anthu; mafumu a anthuwo adzachokera mwa iye.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzamdalitsa iye, ndiponso ndidzakupatsa iwe mwana wamwamuna wobadwa mwa iye, inde, ndidzamdalitsa iye, ndipo adzakhala amace a mitundu, mafumu a anthu adzaturuka mwa iye.