Genesis 17:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Mulungu adati, “Iyai, ndi mkazi wako Sara amene adzakubalira mwana wamwamuna ndipo udzamutcha Isaki. Ndidzasunga chipangano changa ndi iyeyo ndiponso ndi zidzukulu zake, ndipo chipanganocho chidzakhala chamuyaya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mulungu anati, Koma Sara mkazi wako adzakubalira iwe mwana wamwamuna; ndipo udzamutcha dzina lake Isaki; ndipo ndidzalimbikitsa naye pangano langa, kuti likhale pangano la nthawi zonse, la ku mbeu zake za pambuyo pake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Mulungu anati, “Ayi, koma mkazi wako Sara adzakubalira mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha Isake. Ndidzasunga pangano langa losatha ndi iyeyu komanso ndi zidzukulu zobwera pambuyo pake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mulungu anati, Koma Sara mkazi wako adzakubalira iwe mwana wamwamuna; ndipo udzamucha dzina lace Isake; ndipo ndidzalimbikitsa nave pangano langa, kuti likhale pangano la nthawi zonse, la ku mbeu zace za pambuyo pace.