Genesis 17:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma kunena za Ismaeleyu, ndidzamdalitsa, ndipo ndidzampatsa ana ambiri pamodzi ndi zidzukulu. Adzakhala bambo wa mafumu khumi ndi aŵiri, ndipo zidzukulu zake ndidzakhala mtundu waukulu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma za Ismaele, ndamvera iwe: taona, ndamdalitsa iye, ndipo ndidzamchulukitsa iye ndithu; adzabala akalonga khumi ndi awiri, ndipo ndidzamuyesa iye mtundu waukulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma za Ismaeli, ndamva. Ndidzamudalitsadi, ndipo adzakhala ndi zidzukulu zambiri. Iye adzakhala kholo la mafumu khumi ndi awiri ndipo mwa iye mudzatuluka mtundu waukulu wa anthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma za Ismayeli, ndamvera iwe: taona, ndamdalitsa iye, ndipo ndidzamcurukitsa iye ndithu; adzabala akaronga khumi ndi awiri, ndipo ndidzamuyesa iye mtundu waukuru.